Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo yatsindika kuti Namondwe Chido wakula ndipo akuyembekezera kuwomba pa doko la Nakala m’dziko la Mozambique Lamulungu pa 15 December zomwe zitha kudzetsa mvula yochuluka komanso kusefukira kwa madzi m’madera ena a m’dziko muno.
Pachifukwa ichi, Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi ikupempha kuti anthu amene ali mmadera omwe ali pachiopsezo kwambiri ndipo Namondweyu akhoza kulowerako monga Mangochi, Zomba, Phalombe ndi Mulanje atsatire malangizo awa; asamukire mmadera aku mtunda, azitsatira uthenga wa za nyengo, kupewa kuwoloka mitsinje yosefukira, kupewa kuyandikira ma waya a magetsi, kusamutsira katundu ofunika ku malo okwera ndi malangizo ena ambiri.
Kutsatira chenjezeroli, bungwe la Save the Children mogwirizana ndi mabungwe a Beyond Our Hearts Foundation komanso YODEP yayamba kale kuchenjeza anthu za Namondweyu ma boma a Zomba ndi Neno. Bungweli likugwiranso limodzi ntchito ndi Nthambi yoona za Nyengo yi pokonzekera ndi kulimbana ndi zotsatira za Namondweyu.